Acts 10

Kenturiyo Korneliyo Ayitana Petro

1Ku Kaisareya kunali munthu wina dzina lake Korneliyo, mkulu wa asilikali 100 wa gulu la Italiya. 2Iye ndi banja lake lonse amapembedza ndi kuopa Mulungu. Iye amathandiza osowa mowolowamanja ndipo amapemphera kwa Mulungu nthawi zonse. 3Tsiku lina, nthawi ili ngati 3 koloko masana, anaona masomphenya. Anaona bwino ndithu mngelo wa Mulungu, amene anabwera kwa iye ndi kuti, “Korneliyo.”

4Korneliyo anamuyangʼanitsitsa mngeloyo mwa mantha. Iye anafunsa kuti, “Nʼchiyani kodi Ambuye?”

Mngelo anayankha kuti, “Mapemphero ako ndi zachifundo zako zafika pamaso pa Mulungu ngati chikumbutso.
5Tsopano tuma anthu apite ku Yopa kuti akayitane munthu dzina lake Simoni Petro. 6Iye akukhala ndi Simoni mmisiri wa zikopa, amene nyumba yake ili mʼmbali mwa nyanja.”

7Mngeloyo anayankhula naye anachoka, Korneliyo anayitana antchito ake awiri ndiponso msilikali mmodzi wa iwo amene ankamutumikira yemwe ankapembedza Mulungu. 8Iye anawafotokozera zonse zimene zinachitika ndipo anawatuma kuti apite ku Yopa.

Masomphenya a Petro

9Mmawa mwake, nthawi ili ngati 12 koloko anthuwo atayandikira mzindawo, Petro anakwera pa denga kukapemphera. 10Iye anamva njala ndipo anafuna chakudya, ndipo akukonza chakudyacho, iye anachita ngati wakomoka. 11Iye anaona kuthambo kutatsekuka, ndi chinthu china chikutsitsidwa pansi chooneka ngati chinsalu chachikulu chomangidwa pa msonga zake zinayi. 12Mʼmenemo munali nyama zonse zamiyendo inayi pamodzinso ndi zokwawa za dziko lapansi ndiponso mbalame zamlengalenga. 13Petro anamva mawu akuti, “Petro, dzuka, ipha nudye.”

14Petro anayankha kuti, “Ayi, Ambuye! Ine sindinadyepo kanthu kosayeretsedwa kapena konyansa.”

15Petro anamvanso kachiwiri mawu akuti, “Usachiyese chonyansa chimene Mulungu wachiyeretsa.”

16Zimenezi zinachitika katatu ndipo nthawi yomweyo chinsalu chija chinatengedwanso kupita kumwamba.

17Petro akuganizira za tanthauzo la masomphenyawo, anthu amene Korneliyo anawatuma anapeza kumene kunali nyumba ya Simoni ndipo anayima pa chipata. 18Iwo anayitana nafunsa ngati Simoni amene amadziwika ndi dzina loti Petro amakhala kumeneko.

19Petro akuganizirabe za masomphenyawo, Mzimu Woyera anati kwa iye, “Simoni, anthu atatu akukufunafuna. 20Dzuka, tsika. Usakayike upite nawo pakuti ndawatuma ndine.”

21Petro anatsika ndipo anati kwa anthuwo, “Amene mukufunayo ndine. Mwabwera kuno chifukwa chiyani?”

22Anthuwo anayankha kuti, “Ife tachokera kwa Korneliyo, mkulu woyangʼanira asilikali 100. Iye ndi munthu wolungama ndiponso woopa Mulungu, amene amalemekezedwa ndi Ayuda onse. Mngelo woyera anamuwuza kuti mupite ku nyumba yake kuti akamve mawu amene inu mukanene.” 23Pamenepo Petro anawalowetsa mʼnyumba ndipo anawasamala ngati alendo ake. Mmawa mwake Petro ananyamuka napita nawo ndipo abale ena a ku Yopa anapita naye pamodzi.

Petro ku Nyumba ya Korneliyo

24Tsiku linalo Petro anafika ku Kaisareya. Korneliyo anawadikirira ndipo anali atawasonkhanitsa pamodzi abale ake ndi abwenzi ake a pamtima. 25Petro akulowa mʼnyumba, Korneliyo anakumana naye ndipo anadzigwetsa pa mapazi ake namulambira. 26Koma Petro anamuyimiritsa nati, “Imirira, inenso ndine munthu ngati iwe.”

27Akuyankhula naye, Petro analowa mʼnyumba ndipo anapeza gulu lalikulu la anthu litasonkhana. 28Iye anawawuza kuti, “Inu mukudziwa bwino kuti ndi kutsutsana ndi lamulo ngati Myuda ayanjana ndi Mkunja kapena kuyendera wina aliyense wa mtundu wina. Koma Mulungu wandionetsa ine kuti ndisatchule munthu aliyense kuti ndi wosayenera kapena wonyansa. 29Nʼchifukwa chake ndabwera mosawiringula pamene munandiyitana. Tsopano ndikufunseni,” Mwandiyitanira chiyani?

30Komeliyo anayankha kuti, “Masiku anayi apitawo, nthawi yonga yomwe ino, 3 koloko masana ndimapemphera mʼnyumba mwanga. Mwadzidzidzi patsogolo panga panayimirira munthu wovala zovala zonyezimira. 31Ndipo anati, ‘Korneliyo, Mulungu wamva mapemphero ako ndipo wakumbukira mphatso zako kwa osauka. 32Tuma anthu ku Yopa akayitane Simoni wotchedwa Petro. Iye akukhala mʼnyumba ya Simoni mmisiri wazikopa amene amakhala mʼmbali mwa nyanja.’ 33Nʼchifukwa chake ndinatumiza anthu nthawi yomweyo ndipo mwachita bwino kuti mwabwera. Tsopano ife tonse tili pano pamaso pa Mulungu kuti timve zonse zimene Ambuye akukulamulani kuti mutiwuze ife.”

34Ndipo Petro anayamba kuyankhula nati, “Zoonadi, tsopano ndazindikira kuti Mulungu sakondera. 35Koma amalandira anthu a mtundu uli wonse amene amaopa Iye ndiponso kuchita chilungamo. 36Uwu ndi uthenga umene Mulungu anatumiza kwa Aisraeli, kulalikira Uthenga Wabwino wamtendere mwa Yesu Khristu amene ndi Ambuye wa onse. 37Inu mukudziwa zimene zinachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa ubatizo umene Yohane analalikira, 38kuti Mulungu, anamudzoza Yesu, wa ku Nazareti ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu ndiponso mmene Iye anapita nachita zabwino ndi kuchiritsa onse amene anali pansi pa mphamvu ya mdierekezi, popeza kuti Mulungu anali naye.

39“Ife ndife mboni za zonse zimene anachita mʼdziko la Ayuda ndiponso ku Yerusalemu. Anamupha Iye pakumupachika pa mtengo, 40koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa pa tsiku lachitatu, ndipo analola kuti aonekere poyera. 41Iye sanaonekere kwa anthu onse koma kwa mboni zimene Mulungu anazisankhiratu, kwa ife amene timadya ndi kumwa naye atauka kwa akufa. 42Iye anatilamulira ife kuti tilalikire kwa anthu ndi kuchitira umboni kuti Iye ndiye amene Mulungu anamusankha kukhala woweruza wa amoyo ndi akufa. 43Aneneri onse achitira Iye umboni kuti aliyense amene akhulupirira Iye amakhululukidwa machimo chifukwa cha dzina lake.”

44Petro akuyankhulabe mawu amenewa, Mzimu Woyera unatsikira pa onse amene amamva uthengawo. 45Abale a mdulidwe omwe anabwera ndi Petro anadabwa kuona kuti mphatso ya Mzimu Woyera yapatsidwanso kwa anthu a mitundu ina. 46Pakuti anamva iwo akuyankhula mʼmalilime ndi kuyamika Mulungu. Ndipo Petro anati, 47“Kodi alipo amene angawaletse anthu awa kubatizidwa mʼmadzi? Iwotu alandira Mzimu Woyera monga ifenso.” 48Tsono iye analamula kuti abatizidwe mʼdzina la Yesu Khristu. Ndipo anthu aja anamupempha Petro kuti akhale nawo masiku angapo.

Copyright information for NyaCCL